Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 16:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Kora, mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;

2. ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna: mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israyeli, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.

3. Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?

4. Pamene Mose anamva ici anagwa nkhope yace pansi;

5. nanena ndi Kora ndi khamu lace lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ace ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa iye.

6. Citani ici; dzitengereni mbale za zofukiza, Kora, ndi khamu lace lonse;

7. nimuikemo moto, muikenso cofukiza pamenepo, pamaso pa Yehova, mawa; ndipo kudzali kuti amene Yehova amsankha, wopatulika ndiye; mwakula mphamvu, inu ana a Levi.

8. Ndipo Mose ananena ndi Kora, Tamvani tsono, inu ana a Levi;

9. kodi muciyesa cinthu cacing'ono, kuti Mulungu wa Israyeli anakusiyanitsani ku khamu la Israyeli, kukusendezani pafupi pa iye, kucita nchito ya kacisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;

10. ndi kuti anakusendeza iwe, ndi abale ako onse, ana a Levi, pamodzi ndi iwe? ndipo kodi mufunanso nchito ya nsembe?

11. Cifukwa cace, iwe ndi khamu lonse mwasonkhana kutsutsana ndi Yehova; ndipo Aroniyo ndani, kuti mudandaule pa iye?

12. Ndipo Mose anatuma kukaitaniza Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu; koma anati, Sitifikako:

13. kodi ndi cinthu cacing'ono kuti watikweza kuticotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, kutipha m'cipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?

Werengani mutu wathunthu Numeri 16