Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 15:30-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Koma munthu wakucita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo acitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wace.

31. Popeza ananyoza mau a Yehova, nathyola lamulo lace; munthuyu amsadze konse; mphulupulu yace ikhale pa iye.

32. Ndipo pokhala ana a Israyeli m'cipululu, anapeza munthu wakufuna nkhuni tsiku la Sabata.

33. Ndipo amene adampezawo alinkufuna nkhuni anabwera naye kwa Mose ndi Aroni, ndi kwa khamu lonse.

34. Ndipo anathanga wamsunga, popeza sicinanenedwa coyenera kumcitira iye.

35. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Amuphe munthuyu ndithu; khamu lonse limponye miyala kunja kwa cigono.

36. Pamenepo khamu lonse linamturutsa kunja kwa cigono, ndi kumponya miyala, ndipo anafa; monga Yehova adauza Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 15