Koma munthu wakucita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo acitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wace.