Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 15:17-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

18. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Pamene mulowa m'dziko limene ndirikukulowetsani,

19. kudzali, pakudya inu mkate wa m'dzikolo, muzikwezera Yehova nsembe yokweza.

20. Pa mtanda wanu woyamba muperekeko kamtanda, kakhale nsembe yokweza; monga mumacitira nsembe yokweza ya popuntha tirigu, momwemo muzikakweza.

21. Muzipatsa Yehova nsembe yokweza yoitenga ku mtanda wanu woyamba, mwa mibadwo yanu.

22. Ndipo pamene mulakwa, osacita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose;

23. ndizo zonse Yehova anakuuzani ndi dzanja la Mose, kuyambira tsikulo Yehova anauza, ndi kunkabe m'mibadwo yanu;

24. pamenepo kudzali, ngati anacicita osati dala, osacidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya pfungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira, monga mwa ciweruzo cace; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo.

25. Ndipo wansembe azicita cotetezera khamu lonse la ana a Israyeli, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanacita dala, ndipo anadza naco copereka cao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yaucimo pamaso pa Yehova, cifukwa ca kulakwa osati dala.

26. Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli, adzakhululukidwa, ndi mlendo yemwe wakukhala pakati pao; popeza khamu lonse linacicita osati dala.

27. Ndipo akacimwa munthu mmodzi osati dala, abwere nayo mbuzi yamsoti ya caka cimodzi, ikhale nsembe yaucimo.

28. Ndipo wansembe acite comtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumcita comtetezeraj ndipo adzakhululukidwa.

29. Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israyeli, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale naco cilamulo cimodzi kwa iye wakucita kanthu kosati dala.

30. Koma munthu wakucita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo acitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wace.

Werengani mutu wathunthu Numeri 15