Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 14:2-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo ana onse a Israyeli anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Aigupto; kapena mwenzi tikadafa m'cipululu muno!

3. Ndipo Yehova atitengeranii kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala cakudya cao; kodi sikuli bwino tibwerere ku Aigupto?

4. Ndipo anati wina ndi mnzace, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Aigupto.

5. Pamenepo Mose ndi Aroni anagwa nkhope pansi pamaso pa msonkhano wonse wa khamu la ana a Israyeli.

6. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebi mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zobvala zao;

7. nanena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu.

8. Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

9. Cokhaci musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawacokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.

10. Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala, Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'cihema cokomanako kwa ana onse a Israyeli.

11. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, cinkana zizindikilo zonse ndinazicita pakati pao?

12. Ndidzawakantha ndi mliri, ndi kuwacotsera colowa cao, ndipo ndidzakusandutsa iwe mtundu wa anthu waukuru ndi wamphamvu koposa iwowa.

13. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Pamenepo Aaigupto adzamva; popeza munakweza anthu awa ndi mphamvu yanu kuwacotsa pakati pao;

14. ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova, ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku.

15. Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti,

16. Popeza Yehova sanakhoza kuwalowetsa anthu awa m'dziko limene anawalumbirira, cifukwa cace anawapha m'cipululu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 14