Ndipo Yehova atitengeranii kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala cakudya cao; kodi sikuli bwino tibwerere ku Aigupto?