Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 14:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova, ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku.

15. Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti,

16. Popeza Yehova sanakhoza kuwalowetsa anthu awa m'dziko limene anawalumbirira, cifukwa cace anawapha m'cipululu.

17. Ndipo tsopano, ikuletu mphamvu ya Mbuye wanga, monga mudanena, ndi kuti,

18. Yehova ndiye wolekereza, ndi wa cifundo cocuruka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula woparamula; wakuwalanga ana cifukwa ca mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai.

19. Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa cifundo canu cacikuru, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Aigupto kufikira tsopano.

20. Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mau ako:

21. koma ndithu, pali Ine, dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi ulemerero wa Yehova;

22. popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikilo zanga, ndidazicita m'Aigupto ndi m'cipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;

23. sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona;

24. koma mtumiki wanga Kalebi, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zace zidzakhala nalo.

25. Koma Aamaleki ndi Akanani akhala m'cigwamo; tembenukani mawa, nimumke ulendo wanu kucipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

26. Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati,

Werengani mutu wathunthu Numeri 14