Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 13:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira cipululu ca Zini kufikira Rehobo, polowa ku Hamati.

22. Ndipo anakwera njira ya kumwela nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talmai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zoani m'Aigupto.)

23. Ndipo anadza ku cigwa ca Esikolo, nacekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.

24. Malowa anawacha cigwa ca Esikolo, cifukwa ca tsangolo ana a lsrayeli analicekako.

25. Pamenepo anabwerera atazonda dziko, atatha masiku makumi anai.

26. Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israyeli, ku cipululu ca Parana ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.

27. Ndipo anafotokozera, nati, Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu a moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ndi zipatso zace siizi.

28. Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikuru ndithu: ndipo tinaonakonso ana a Anaki.

29. Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordano.

Werengani mutu wathunthu Numeri 13