Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 10:27-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Nafitali anayang'anira Ahira mwana wa Enani.

28. Potero maulendo a ana a Israyeli anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendowao.

29. Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reueli Mmidyani mpongozi wa Mose, Ife tirikuyenda kumka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakucitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israyeli zokoma.

30. Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga.

31. Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m'cipululu, ndipo udzakhala maso athu.

32. Ndipo kudzatero, ukamuka nafe, inde, kudzali kuti zokoma ziri zonse Yehova aticitira ife, zomwezo tidzakucitira iwe.

33. Ndipo anayenda kucokera ku phiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la cipangano ca Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.

34. Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kucokera kucigono.

35. Ndipo kunali pakucoka kumka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.

36. Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwi zikwi za Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Numeri 10