1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2. Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ace; ucite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m'zigono.
3. Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la cihema cokomanako,
4. Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akuru a zikwi a m'Israyeli, azisonkhana kuli iwe.
5. Mukaliza cokweza, ayende a m'zigono za kum'mawa.
6. Mukalizanso cokweza, a m'zigono za kumwela ayende; alize cokweza pakumuka.
7. Pomemeza msonkhano mulize, wosati cokweza ai.
8. Ana amuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu.
9. Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kucita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize cokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukila inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.