Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 7:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ana a dziko amene anakwera kucokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babulo adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense ku mudzi wace, ndi awa:

7. ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Moredekai, Bilisani, Misiperete, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisrayeli ndiwo:

8. ana a Parosi zikwi ziwiri mphambu zana limodzi kudza makumi asanu ndi awiri.

9. Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

10. Ana a Ara, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

11. Ana a Pakati Moabu, a ana a Yesuwa ndi Yoabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi limodzi ndi asanu ndi atatu.

12. Ana a Elamu, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai.

13. Ana a Zatu, mazana asanu ndi atatu mphambu makumi anai kudza asanu.

14. Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

15. Ana a Binui, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 7