Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufuru, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa cibadwidwe cao. Ndipo ndinapeza buku la cibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo.