Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 6:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wace kwa ine kacisanu, ndi kalata wosatseka m'dzanja mwace;

6. m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gasimu acinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; cifukwa cace mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa.

7. Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.

8. Koma ndinamtumizira mau, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako.

9. Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka nchito, ndipo siidzacitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.

10. Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane ku nyumba ya Mulungu m'kati mwa Kacisi, titsekenso pa makomo a Kacisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 6