m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gasimu acinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; cifukwa cace mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa.