Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 4:19-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo ndinati kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Nchito ndiyo yocuruka ndi yacitando, ndi ife tiri palace palace palingapo, yense azana ndi mnzace;

20. pali ponse mukumva mau a lipenga, musonkhanire komweko kwa ife; Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo.

21. Momwemo tinalikugwira nchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbanda kuca mpaka zaturuka nyenyezi.

22. Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Ali yense agone m'Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wace, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira nchito usana.

23. Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anabvula zobvala zace, yense anapita ndi cida cace kumadzi.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 4