Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anabvula zobvala zace, yense anapita ndi cida cace kumadzi.