Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 2:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo ndinati kwa mfumu, Cikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda ku mudzi wa manda a makolo anga, kuti ndiumange.

6. Ninena nane mfumu, irikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wace wamkuru, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaichula nthawi.

7. Ndinanenanso kwa mfumu, Cikakomera mfumu, indipatse akalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda;

8. ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya ku zipata, za linga liri kukacisi, ndi ya linga la mudzi, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira.

9. Ndinafika tsono kwa ziwanga za tsidya lino la mtsinje, ndipo ndinawapatsa akalata a mfumu. Koma mfumu idatumiza apite nane akazembe a nkhondo, ndi apakavalo.

10. Atamva Sanibalati Mhoroni, ndi Tobiya kapoloyo M-amoni, cidawaipira kwakukuru, kuti wadza munthu kuwafunica ana a Israyeli cokoma.

11. Motero ndinafika ku Yerusalemu, ndi kukhalako masiku atatu.

12. Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine coika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndicitire Yerusalemu; panalibenso nyama yina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.

13. Ndipo ndinaturuka usiku pa cipata ca kucigwa, kumka ku citsime ca cinjoka, ndi ku cipata ca kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zace zothedwa ndi moto.

14. Ndipo ndinapitima kumka ku cipata cacitsime, ndi ku dziwe la mfumu; koma popita nyama iri pansi panga panaicepera.

15. Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang'ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa cipata ca kucigwa, momwemo ndinabwereranso.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 2