Ndipo ndinaturuka usiku pa cipata ca kucigwa, kumka ku citsime ca cinjoka, ndi ku cipata ca kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zace zothedwa ndi moto.