Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 13:20-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Momwemo eni malonda ndi ogulitsa malonda ali onse, anagona kunja kwa Yerusalemu kamodzi kapena kawiri.

21. Koma ndinawacima umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikanso pa Sabata.

22. Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula dzuwa la Sabata. Mundikumbukire Icinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa cifundo canu cacikuru.

23. Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amoabu,

24. ndi ana ao analankhula mwina Ciasidodi, osadziwitsa kulankhula Ciyuda, koma monga umo amalankhula mtundu wao uli wonse.

25. Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna, kapena a inu nokha, ana ao akazi.

26. Nanga Solomo mfumu ya Israyeli sanacimwa nazo zinthu izi? cinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wace anamkonda, ndi Mulungu wace anamlonga mfumu ya Aisrayeli onse; koma ngakhale iye, akazi acilendo anamcimwitsa.

27. Ndipo kodi tidzamvera inu, kucita coipa ici cacikuru conse, kulakwira Mulungu wathu ndi kudzitengera akazi acilendo?

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 13