Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 13:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo kunali, kukadayamba cizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu dzuwa la Sabata.

20. Momwemo eni malonda ndi ogulitsa malonda ali onse, anagona kunja kwa Yerusalemu kamodzi kapena kawiri.

21. Koma ndinawacima umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikanso pa Sabata.

22. Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula dzuwa la Sabata. Mundikumbukire Icinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa cifundo canu cacikuru.

23. Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amoabu,

24. ndi ana ao analankhula mwina Ciasidodi, osadziwitsa kulankhula Ciyuda, koma monga umo amalankhula mtundu wao uli wonse.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 13