Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 12:23-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ana a Levi, akuru a nyumba za makolo, analembedwa m'buku la macitidwe, mpaka masiku a Yohanana mwana wa Eliasibu.

24. Ndi akuru a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyeli, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.

25. Mataniya, ndi Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni, Akubi, ndiwo odikira akulonda pa nyumba za cuma ziri kuzipata.

26. Awa anakhala m'masiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndi m'masiku a Nehemiya kazembe, ndi a Ezara wansembe mlembiyo.

27. Ndipo popereka linga la Yerusalemu anafunafuna Alevi m'malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti acite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuyimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze.

28. Ana a oyimbirawo anasonkhana ocokera ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku midzi ya Anetofati,

29. ndi ku Betegiligala, ndi ku minda ya Geba ndi Azimaveti; popeza oyimbirawo adadzimangira midzi pozungulira Yerusalemu.

30. Ndipo ansembe ndi Alevi anadziyeretsa okha, nayeretsa anthu, ndi zipata, ndi linga.

31. Pamenepo ndinakwera nao akuru a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akuru oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kumka ku cipata ca kudzala;

32. ndi pambuyo pao anayenda Hosaya, ndi limodzi la magawo awiri a akuru a Yuda,

33. ndi Azariya, Ezara ndi Mesulamu,

34. Yuda, ndi Benjamini, ndi Semaya, ndi Yeremiya,

35. ndi ana ena a ansembe ndi malipenga: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,

36. ndi abale ace: Semaya, ndi Azareli, Milalai, Gilelai, Maai, Netaneli, ndi Yuda, Hanani, ndi zoyimbira za Davide munthu wa Mulungu; ndi Ezara mlembiyo anawatsogolera;

37. ndi ku cipata ca kucitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mudzi wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku cipata ca kumadzi kum'mawa.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 12