Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 10:30-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. ndi kuti sitidzapereka ana athu akazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu amuna ana ao akazi;

31. ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, dzuwa la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao dzuwa la Sabata, kapena dzuwa lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka caka cacisanu ndi ciwiri ndi mangawa ali onse.

32. Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka caka ndi caka limodzi la magawo atatu a sekeli ku nchito ya nyumba ya Mulungu wathu;

33. kuliperekera mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israyeli zoipa, ndi nchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.

34. Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a copereka ca nkhuni, kubwera nazo ku nyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika caka ndi caka, kuzisonkha pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'cilamulo;

35. ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uli wonse caka ndi caka, ku nyumba ya Yehova;

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 10