Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 1:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Mukumbukile mau mudalamulira mtumiki wanu Mose, ndi kuti, Mukalakwa, ndidzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu;

9. koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwacita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kucokera komweko, ndi kubwera nao ku malo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa.

10. Ndipo awa ndi akapolo anu ndi anthu anu, amene munawaombola ndi mphamvu yanu yaikuru, ndi dzanja lanu lolimba.

11. Yehova, mucherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mulemereze kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera cifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu cakumwa cace.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 1