11. Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe atamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwace.
12. Pakuti munthu sadziwatu mphindi yace; monga nsomba zigwidwa m'ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.
13. Ndaonanso nzeru pansi pano motero, ndipo inandionekera yaikuru;
14. panali mudzi waung'ono muli anthu owerengeka; ndipo inadzako mfumu yaikuru, niizinga ndi nkhondo, nimangapo malinga akuru;
15. koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mudziwo ndi nzeru yace; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.
16. Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ace.
17. Mau a anzeru acete amveka koposa kupfuula kwa wolamulira mwa zitsiru.
18. Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wocimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.