Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 3:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zaipa; ndi malo a cilungamo, komweko kuli zoipa.

17. Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi nchito zonse.

18. Ndinati mumtima mwanga, kuti izi zicitika ndi ana a anthu, kuti Mulungu awayese ndi kuti akazindikire eni ace kuti ndiwo nyama za kuthengo.

19. Pakuti comwe cigwera ana a anthu cigweranso nyamazo; ngakhale cowagwera ncimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi cabe,

20. onse apita ku malo amodzi; onse acokera m'pfumbi ndi onse abweranso kupfumbi.

21. Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wakwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?

22. M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi nchito zace; pakuti gawo lace ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona comwe cidzacitidwa ataca iyeyo?

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 3