Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 3:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Cinthu ciri conse anacikongoletsa pa mphindi yace; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse nchito Mulungu wazipanga ciyambire mpaka citsiriziro.

12. Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kucita zabwino pokhala ndi moyo.

13. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m'nchito zace zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.

14. Ndidziwa kuti zonse Mulungu azicita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kucotsapo; Mulungu nazicita kuti anthu akaope pamaso pace.

15. Cocomwe cinaoneka, cirikuonekabe; ndi comwe cidzaoneka cinacitidwa kale; Mulungu anasanthula zocitidwa kale.

16. Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zaipa; ndi malo a cilungamo, komweko kuli zoipa.

17. Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi nchito zonse.

18. Ndinati mumtima mwanga, kuti izi zicitika ndi ana a anthu, kuti Mulungu awayese ndi kuti akazindikire eni ace kuti ndiwo nyama za kuthengo.

19. Pakuti comwe cigwera ana a anthu cigweranso nyamazo; ngakhale cowagwera ncimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi cabe,

20. onse apita ku malo amodzi; onse acokera m'pfumbi ndi onse abweranso kupfumbi.

21. Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wakwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?

22. M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi nchito zace; pakuti gawo lace ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona comwe cidzacitidwa ataca iyeyo?

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 3