Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 2:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Pakuti wanzerusaposa citsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo, Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati citsirutu.

17. Cifukwa cace ndinada moyo; pakuti nchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi cabe ndi kungosautsa mtima.

18. Ndipo ndinada nchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno; pakuti ndidzamsiyira izo munthu wina amene adzanditsata.

19. Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena citsiru? Koma adzalamulira nchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Icinso ndi cabe.

20. Ndipo ndinatembenuka ndi kukhululuka za nchito zanga zonse ndasauka nazo kunja kuno.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 2