1. Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi cimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, icinso ndi cabe.
2. Ndinati, Kuseka ndi misala; ndi cimwemwe kodi cicita ciani?
3. Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire cabwinoco ca ana a anthu nciani cimene azicicita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.
4. Ndinadzipangira zazikuru; ndinadzimangira nyumba; ndi kunka mipesa;
5. ndinakonza mphanie ndi minda yanga, ndi kuokamo mitengo ya zipatso za mitundu mitundu;
6. ndinadzipangira ndekha matamanda a madzi akuthirira madzi m'nkhalango momeramo mitengo;
7. ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikuru ndi zazing'ono kupambana onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine;
8. ndinakundikanso siliva ndi golidi ndi cuma ca mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuyimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoyimbira za mitundu mitundu.
9. Ndinakula cikulire kupambana onse anali m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe.
10. Ndipo ciri conse maso anga anacifuna sindinawamana; sindinakaniza mtima wanga cimwemwe ciri conse pakuti mtima wanga unakondwera ndi nchito zanga zonse; gawo langa la m'nchito zanga zonse ndi limeneli.
11. Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi nchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zacabecabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.
12. Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angacite ciani? Si comwe cinacitidwa kale.
13. Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.