Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 7:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kalanga ine! pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wamphesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.

2. Watha wacifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wace ndi ukonde.

3. Manja ao onse awiri agwira coipa kucicita ndi cangu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza cifukwa ca mphotho; ndi wamkuruyo angonena cosakaza moyo wace; ndipo aciluka pamodzi.

4. Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao.

5. Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.

6. Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amace, mpongozi aukira mpongozi wace; adani ace a munthu ndiwo a m'nyumba yace.

7. Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa cipulumutso canga; Mulungu wanga adzandimvera.

8. Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.

9. Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, cifukwa ndamcimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditurutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya cilungamo cace.

10. Pamenepo mdani wanga adzaciona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.

11. Tsiku lakumanga malinga ako, tsiku lomwelo lembalo lidzacotsedwa kunka kutali.

12. Tsiku lomwelo adzadza kwa iwe, kucokera ku Asuri ndi midzi ya ku Aigupto, kuyambira ku Aigupto kufikira ku Mtsinje, ndi kuyambira kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuyambira kuphiri kufikira kuphiri.

13. Koma dziko lidzakhala labwinja cifukwa ca iwo okhalamo, mwa zipatso za macitidwe ao.

Werengani mutu wathunthu Mika 7