Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 6:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tamverani tsono conena Yehova: Nyamuka, tsutsana nao mapiri, ndi zitunda zimve mau ako.

2. Tamvani, mapiri inu, citsutsano ca Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali naco citsutsano ndi anthu ace, ndipo adzatsutsana ndi Israyeli.

3. Anthu anga inu, ndakucitirani ciani? ndakulemetsani ndi ciani? citani umboni wonditsutsa.

4. Pakuti ndinakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriamu.

Werengani mutu wathunthu Mika 6