Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 2:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; mucotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha.

10. Nyamukani, cokani, pakuti popumula panu si pano ai; cifukwa ca udio Wakuononga ndi cionongeko cacikuru.

11. Munthu akayenda ndi mtima wacinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi cakumwa cakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ace.

12. Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israyeli; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Boma; ngati zoweta pakati pa busa pao adzacita phokoso cifukwa ca kucuruka anthu.

13. Wotyola wakwera pamaso pao; iwo anatyola, napita kucipata, naturuka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.

Werengani mutu wathunthu Mika 2