Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Mau akutsutsa akulanda za eni

1. Tsoka iwo akulingirira cinyengo, ndi kukonza coipa pakama pao! kutaca m'mawa acicita, popeza cikhozeka m'manja mwao.

2. Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazicotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yace, inde munthu ndi colowa cace.

3. Cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndilingirira coipa pa banja ili, cimene simudzacotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; Pakuti nyengo iyi ndi yoipa.

4. Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! andicotsera ili! agawira opikisana minda yathu.

5. Cifukwa cace udzasowa woponya cingwe camaere m'msonkhano wa Yehova.

6. Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzacoka.

7. Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? izi ndi nchito zace kodi? Mau anga samcitira zokoma kodi, iye amene ayenda coongoka?

8. Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula copfunda ku maraya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.

9. Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; mucotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha.

10. Nyamukani, cokani, pakuti popumula panu si pano ai; cifukwa ca udio Wakuononga ndi cionongeko cacikuru.

11. Munthu akayenda ndi mtima wacinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi cakumwa cakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ace.

12. Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israyeli; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Boma; ngati zoweta pakati pa busa pao adzacita phokoso cifukwa ca kucuruka anthu.

13. Wotyola wakwera pamaso pao; iwo anatyola, napita kucipata, naturuka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.