Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 1:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Cicitika ici conse cifukwa ca kulakwa kwa Yakobo, ndi macimo a nyumba ya Israyeli. Kulakwa kwa Yakobo nkotani? Si ndiko Samariya? ndi misanje ya Yuda ndi iti? si ndiyo Yerusalemu?

6. Cifukwa cace ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wamphesa; ndipo ndidzataya miyala yace m'cigwa, ndi kufukula maziko ace.

7. Ndi mafano ace osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zace zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ace onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi waciwerewere, ndipo zidzabwerera ku mphotho ya mkazi waciwerewere.

8. Cifukwa ca ici ndidzacita maliro, ndi kucema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamarisece; ndidzalira ngati mimbulu, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.

9. Pakuti mabala ace ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku cipata ca anthu anga, ku Yerusalemu.

10. Musacifotokoza m'Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'pfumbi.

11. Pitiratu, wokhala m'Safiri iwe, wamarisece ndi wamanyazi; wokhala m'Zanana sanaturuka; maliro a Betezeli adzakulandani pokhala pace.

12. Pakuti wokhala m'Maroti alindira cokoma, popeza coipa catsika kwa Yehova kumka ku cipata ca Yerusalemu.

13. Manga gareta ku kavalo waliwiro, wokhala m'Lakisi iwe, woyamba kucimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israyeli zinapezedwa mwa iwe.

14. Cifukwa cace pereka mphatso zolawirana kwa Moreseti Gati; nyumba za Akizibi zidzakhala cinthu cabodza kwa mafumu a Israyeli.

15. Ndidzakutengeranso wokhala m'Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale colowa cace; ulemerero wa Israyeli udzafikira ku Adulamu.

16. Udziyeseze wadazi, udzimete wekha cifukwa ca ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakucokera, nalowa ndende.

Werengani mutu wathunthu Mika 1