Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 1:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse ziri m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye m'Kacisi wace wopatulika.

3. Pakuti, taonani, Yehova alikuturuka m'malo mwace, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi.

4. Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang'ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetseremba.

5. Cicitika ici conse cifukwa ca kulakwa kwa Yakobo, ndi macimo a nyumba ya Israyeli. Kulakwa kwa Yakobo nkotani? Si ndiko Samariya? ndi misanje ya Yuda ndi iti? si ndiyo Yerusalemu?

6. Cifukwa cace ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wamphesa; ndipo ndidzataya miyala yace m'cigwa, ndi kufukula maziko ace.

7. Ndi mafano ace osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zace zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ace onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi waciwerewere, ndipo zidzabwerera ku mphotho ya mkazi waciwerewere.

8. Cifukwa ca ici ndidzacita maliro, ndi kucema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamarisece; ndidzalira ngati mimbulu, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.

9. Pakuti mabala ace ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku cipata ca anthu anga, ku Yerusalemu.

10. Musacifotokoza m'Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'pfumbi.

11. Pitiratu, wokhala m'Safiri iwe, wamarisece ndi wamanyazi; wokhala m'Zanana sanaturuka; maliro a Betezeli adzakulandani pokhala pace.

12. Pakuti wokhala m'Maroti alindira cokoma, popeza coipa catsika kwa Yehova kumka ku cipata ca Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Mika 1