Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 90:11-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani,Ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?

12. Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero,Kuti tikhale nao mtima wanzeru.

13. Bwerani, Yehova; kufikira liti?Ndipo alekeni atumiki anu.

14. Mutikhutitse naco cifundo canu m'mawa;Ndipo tidzapfuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.

15. Tikondweretseni monga mwa masiku mudatizunzawa,Ndi zaka tidaona coipa.

16. Cocita Inu cioneke kwa atumiki anu,Ndi ulemerero wanu pa ana ao.

17. Ndipo cisomo cace ca Yehova Mulungu wathu cikhale pa ife;Ndipo mutikhazikitsire ife nchito ya manja athu;Inde, nchito ya manja athu muikhazikitse.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 90