Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 6:2-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Mundicitire cifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine:Mundicize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.

3. Moyo wanganso wanthunthumira kwakukuru;Ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?

4. Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga;Ndipulumutseni cifukwa ca kukoma mtima kwanu.

5. Pakuti muimfa m'mosakumbukila Inu:M'mandamo adzakuyamikani dani?

6. Ndalema nako kuusa moyo kwanga;Ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse;Mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.

7. Lapuwala diso langa cifukwa ca cisoni;Lakalamba cifukwa ca onse akundisautsa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 6