Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 53:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu,Kuti aone ngati aliko wanzeru, Wakufuna Mulungu.

3. Onse anabwerera; anabvunda mtima pamodzi;Palibe mmodzi wakucita bwino, nnena mmodzi.

4. Kodi ocita zopanda pace sadziwa?Pomadya anthu anga monga akudya mkate;Ndipo saitana Mulungu.

5. Pamenepo anaopa kwakukuru, popanda cifukwa ca kuopa:Pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe;Unawacititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.

6. Ha, cipulumutso ca Israyeli cicokere m'Ziyoni!Pakubweretsa Mulungu anthu ace a m'ndende,Yakobo adzakondwera, Israyeli adzasekera.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 53