Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 51:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Onani, ndinabadwa m'mphulupulu:Ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.

6. Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo;Ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.

7. Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera;Munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala.

8. Mundimvetse cimwemwe ndi kusekera:Kuti mafupawo munawatyola akondwere.

9. Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga,Ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.

10. Mundilengere mtima woyera, Mulungu;Mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.

11. Musanditaye kundicotsa pamaso panu;Musandicotsere Mzimu wanu Woyera.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 51