Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 44:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira,Za nchitoyo mudaicita masiku ao, masiku akale.

2. Inu munapitikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka;Munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa,

3. Pakuti sanalanda dziko ndi lupanga lao,Ndipo mkono wao sunawapulumutsa:Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu.Popeza munakondwera nao,

4. Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu:Lamulirani cipulumutso ca Yakobo.

5. Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe:M'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.

6. Pakuti sinditama uta wanga,Ndipo lupanga langa silingandipulumutse.

7. Koma Inu munatipulumutsa kwa iwo akutsutsana nafe,Ndipo akudana nafe, mudawacititsa manyazi.

8. Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse,Ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 44