Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 40:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndalalikira cilungamo mu msonkano waukuru;Onani, sindidzaletsa milomo yanga,Mudziwa ndinu Yehova.

10. Cilungamo canu sindinacibisa m'kati mwamtima mwanga;Cikhulupiriko canu ndi cipulumutso canu ndinacinena;Cifundo canu ndi coonadi canu sindinacibisira msonkhano waukuru.

11. Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu:Cifundo canu ndi coonadi canu zindisunge cisungire.

12. Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga,Zocimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya;Ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandicokera mtima.

13. Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni:Fulumirani kudzandithandiza, Yehova.

14. Acite manyazi nadodomeIwo akulondola moyo wanga kuti auononge:Abwerere m'mbuyo, nacite manyazi iwo okondwera kundicitira coipa.

15. Apululuke, mobwezera manyazi aoAmene anena nane, Hede, hede.

16. Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu:Iwo akukonda cipulumutso canu asaleke kunena, Abuke Yehova.

17. Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi;Koma Ambuye andikumbukila ine:Inu ndinu mthandizi wanga, ndi mpulumutsi wanga:Musamacedwa, Mulungu wanga,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 40