Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 39:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndinati, Ndidzasunga njira zanga,Kuti ndingacimwe ndi lilime langa:Ndidzasunga pakamwa panga ndi cam'kamwa,Pokhala woipa ali pamaso panga.

2. Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala cete osalawa cokoma;Ndipo cisoni canga cinabuka.

3. Mtima wanga unatentha m'kati mwaine;Unayaka moto pakulingirira ine:Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa:

4. Yehova, mundidziwitse cimariziro canga,Ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati;Ndidziwe malekezero anga,

5. Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja;Ndipo zaka zanga ziri ngati cabe pamaso panu:Indedi munthu ali yense angakhale wokhazikika, ali cabe konse.

6. Indedi munthu ayenda ngati mthunzi:Indedi abvutika cabe:Asonkhanitsa cuma, ndipo sadziwa adzacilandira ndani?

7. Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira ciani?Ciyembekezo canga ciri pa Inu.

8. Ndipulumutseni kwa zolakwa zangazonse:Musandiike ndikhale cotonza ca wopusa.

9. Ndinakhala du, sindinatsegula pakamwa panga;Cifukwa inu mudacicita.

10. Mundicotsere cobvutitsa canu;Pandithera ine cifukwa ca kulanga kwa dzanja lanu.

11. Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula cifukwa ca mphulupulu,Mukanganula kukongola kwace monga mumacita ndi kadzoce:Indedi, munthu ali yense ali cabe.

12. Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo cherani khutu kulira kwanga;Musakhale cete pa misozi yanga:Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu,Wosakhazikika, monga makolo anga onse.

13. Ndiloleni, kuti nditsitsimuke,Ndisanamuke ndi kukhala kuli zi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 39