Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 39:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndinati, Ndidzasunga njira zanga,Kuti ndingacimwe ndi lilime langa:Ndidzasunga pakamwa panga ndi cam'kamwa,Pokhala woipa ali pamaso panga.

2. Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala cete osalawa cokoma;Ndipo cisoni canga cinabuka.

3. Mtima wanga unatentha m'kati mwaine;Unayaka moto pakulingirira ine:Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa:

4. Yehova, mundidziwitse cimariziro canga,Ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati;Ndidziwe malekezero anga,

5. Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja;Ndipo zaka zanga ziri ngati cabe pamaso panu:Indedi munthu ali yense angakhale wokhazikika, ali cabe konse.

6. Indedi munthu ayenda ngati mthunzi:Indedi abvutika cabe:Asonkhanitsa cuma, ndipo sadziwa adzacilandira ndani?

7. Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira ciani?Ciyembekezo canga ciri pa Inu.

8. Ndipulumutseni kwa zolakwa zangazonse:Musandiike ndikhale cotonza ca wopusa.

9. Ndinakhala du, sindinatsegula pakamwa panga;Cifukwa inu mudacicita.

10. Mundicotsere cobvutitsa canu;Pandithera ine cifukwa ca kulanga kwa dzanja lanu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 39