Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 28:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu,Pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.

3. Musandikoke kundicotsa pamodzi ndi oipa,Ndi ocita zopanda pace;Amene alankhula zamtendere ndi anansi ao,Koma mumtima mwao muli coipa.

4. Muwapatse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa coipa cocita iwo:Muwapatse monga mwa macitidwe a manja ao;Muwabwezere zoyenera iwo.

5. Pakuti sasamala nchito za Yehova,Kapena macitidwe a manja ace,Adzawapasula, osawamanganso.

6. Wodalitsika Yehova,Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.

7. Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi cikopa canga;Mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza:Cifukwa cace mtima wanga ukondwera kwakukuru;Ndipo ndidzamyamika nayo Nyimbo yanga.

8. Yehova ndiye mphamvu yao,Inde mphamvu ya cipulumutso ca wodzozedwa wace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 28