1. Kwa Inu, Yehova, ndidzapfuulira;Thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva:Pakuti ngati munditontholera ine,Ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
2. Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu,Pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.
3. Musandikoke kundicotsa pamodzi ndi oipa,Ndi ocita zopanda pace;Amene alankhula zamtendere ndi anansi ao,Koma mumtima mwao muli coipa.
4. Muwapatse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa coipa cocita iwo:Muwapatse monga mwa macitidwe a manja ao;Muwabwezere zoyenera iwo.
5. Pakuti sasamala nchito za Yehova,Kapena macitidwe a manja ace,Adzawapasula, osawamanganso.
6. Wodalitsika Yehova,Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.
7. Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi cikopa canga;Mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza:Cifukwa cace mtima wanga ukondwera kwakukuru;Ndipo ndidzamyamika nayo Nyimbo yanga.
8. Yehova ndiye mphamvu yao,Inde mphamvu ya cipulumutso ca wodzozedwa wace.