Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 27:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pondifika ine ocita zoipa kudzadya mnofu wanga,Inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.

3. Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,Mtima wanga sungacite mantha:Ingakhale nkhondo ikandiukira,Nde pomweponso ndidzakhulupira,

4. Cinthu cimodzi ndinacipempha kwa Yehova, ndidzacilondola ici:Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,Kupenya kukongola kwace kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kacisi wace.

5. Cifukwa kuti pa dzuwa la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwace:Adzandibisa m'tsenjezi mwa cihema cace;Pathanthwe adzandikweza.

6. Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga;Ndipo ndidzapereka m'cihema mwace nsembe za kupfuula mokondwera;Ndidzayimba, inde, ndidzayimbira Yehova zomlemekeza.

7. Imvani, Yehova, liu langa popfuula ine:Mundicitirenso cifundo ndipo mundibvomereze.

8. Pamene munati, Punani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu:Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.

9. Musandibisire ine nkhope yanu;Musacotse kapolo wanu ndi kukwiya:Inu munakhala thandizo langa;Musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa cipulumutso canga,

10. Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga,Koma Yehova anditola.

11. Mundiphunzitse njira yanu, Yehova,Munditsogolere pa njira yacidikha,Cifukwa ca adani anga,

12. Musandipereke ku cifuniro ca akundisautsa;Cifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zaciwawa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 27