Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 27:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova ndiye kuunika kwanga ndi cipulumutso canga; ndidzaopa yani?Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzacita mantha ndi yani?

2. Pondifika ine ocita zoipa kudzadya mnofu wanga,Inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.

3. Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,Mtima wanga sungacite mantha:Ingakhale nkhondo ikandiukira,Nde pomweponso ndidzakhulupira,

4. Cinthu cimodzi ndinacipempha kwa Yehova, ndidzacilondola ici:Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,Kupenya kukongola kwace kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kacisi wace.

5. Cifukwa kuti pa dzuwa la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwace:Adzandibisa m'tsenjezi mwa cihema cace;Pathanthwe adzandikweza.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 27