Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 23:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.

2. Andigonetsa ku busa lamsipu:Anditsogolera ku madzi ndikha.

3. Atsitsimutsa moyo wanga;Anditsogolera m'mabande a cilungamo, cifukwa ca dzina lace.

4. Inde, ndingakhale ndiyenda m'cigwa ca mthunzi wa Imfa,Sindidzaopa coipa; pakuti Inu muli ndi ine:Cibonga canu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine,

5. Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga:Mwandidzoza mutu wanga mafuta; cikho canga cisefuka.

6. Inde ukoma ndi cifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga:Ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 23