Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 139:15-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika,Poombedwa ine monga m'munsi mwace mwa dziko lapansi.

16. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya,Ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu,Masiku akuti ziumbidwe, Pakalibe cimodzi ca izo.

17. Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wace ndithu!Mawerengedwe ace ndi ambirimbiri!

18. Ndikaziwerenga zicuruka koposa mcenga:Ndikauka ndikhalanso nanu.

19. Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu:Ndipo amuna inu nkhumba mwazi, cokani kwa ine.

20. Popeza anena za Inu moipa,Ndi adani anu achula dzina lanu mwacabe.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 139