4. Wathifula uta wace ngati mdani, waima ndi dzanja lace lamanja ngati mmaliwongo;Wapha onse okondweretsa maso;Watsanulira ukali wace ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.
5. Yehova wasanduka mdani, wameza Israyeli;Wameza zinyumba zace zonse, wapasula malinga ace;Nacurukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi cibumo.
6. Wacotsa mwamphamvu dindiro lace ngati la m'munda;Waononga mosonkhanira mwace;Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi sabata m'Ziyoni;Wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.
7. Ambuye wataya guwa lace la nsembe, malo ace opatulika amnyansira;Wapereka m'manja a adani ace makoma a zinyumba zace;Iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.
8. Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni;Watambalika cingwe, osabweza dzanja lace kuti lisaonongepo;Waliritsa chemba ndi linga; zilefuka pamodzi.
9. Zipata zace zalowa pansi; waononga ndi kutyola mipiringidzo yace;Mfumu yace ndi akalonga ace ali pakati pa amitundu akusowa cilamulo;Inde, aneneri ace samalandira masomphenya kwa Yehova.
10. Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola;Aponya pfumbi pa mitu yao, namangirira ciguduli m'cuuno mwao:Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.
11. Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka;Ciwindi canga cagwa pansi cifukwa ca kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga;Cifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.
12. Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti?Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu,Potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.
13. Ndikucitire umboni wotani? ndikuyerekeze ndi ciani, mwana wamkazi wa Yerusalemu?Ndikulinganize ndi ciani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?Popeza akula ngati nyanja; ndani angakucize?
14. Aneneri ako anakuonera masomphenya acabe ndi opusa;Osaulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako,Koma anakuonera manenero acabe ndi opambutsa.
15. Onse opita panjira akuombera manja:Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati,Kodi uwu ndi mudzi wochedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?
16. Adani ako onse ayasamira pa iwe, Atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza;Ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.