Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Malaki 3:7-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Kuyambira masiku a makolo anu mwapambuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?

8. Kodi munthu adzalanda za Mulungu? ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzi limodzi la magawo khumi, ndi zopereka.

9. Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse.

10. Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale cakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.

11. Ndipo ndidzadzudzula zolusa cifukwa ca inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zace, zosaca m'munda, ati Yehova wa makamu.

12. Ndipo amitundu onse adzacha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, ati Yehova wa makamu.

13. Mau anu andilimbira, ati Yehova. Koma inu mukuti, Tanena motsutsana nanu ndi ciani?

14. Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa cabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wace, ndi kuyenda obvala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?

15. Ndipo tsopano tiwacha odzikuza odala, inde iwo ocita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.

16. Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzace; ndipo Yehova anawachera khutu namva, ndi buku la cikumbutso linalembedwa pamaso pace, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukila dzina lace.

17. Ndipo adzakhala anga anga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wace womtumikira.

18. Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.

Werengani mutu wathunthu Malaki 3